Перейти к основному содержанию

page search

Library Lamulo la Malo

Lamulo la Malo

Lamulo la Malo
AMAKOLO, 2016
LAMULO LA MALO

Resource information

Date of publication
февраля 2020
Resource Language
Pages
32

Translation of the Customary

GAWO I – MAYAMBIDWE NDI KUGWIRITSA NTCHITO KWA LAMULO 1. Lamulo ili ndi Lamulo la Malo Amakolo, 2016. GAWO II – KAYANG’ANIRIDWE KA MALO AMAKOLO 2. Malo amakolo ndi malo onse amene– a) ali mudera lomwe limayang’aniridwa ndi Mfumu ya Ndodo; b) malire ake anakhazikitsidwa ndi Komiti yoyang’anira malo amakolo ku dera-lo; kapena c) ali ndi chiphaso choperekedwa ndi Mkulu woyang’anira za Malo mu Unduna wa za Malo. 3. (1) Chiphaso cha malo amakolo a) chiperekedwe mu dzina la Mfumu ya Ndodo; b) chimapereka mphamvu kwa Komiti yoyamg’anira za malo amakolo pakayendetsedwe ka malowo; c) chimapereka umboni kuti anthu wonse amene ali pa malo amakolowo ndiwololedwa kukhala pamalowo motsatira mwambo waderalo. (2) Mfumu ya Ndodo yili ndi udindo wosunga chiphaso cha dera lake mosamala.  (3) Malire a malo amene ali pansi pa ulamuliro wa Mfumu ya Ndodo sangasinthidwe popanda chilolezo cha Mkulu woyang’anira za malo ku Unduna wa za Malo. (4) Mkulu woyang’anira za malo ku Unduna wa za Malo ali ndi udindo wosunga kalembera wa malo onse amene ali pa ulamuliro wa Mfumu ya Ndodo.

 

 

Land Act, 2016 and the Customary

Land Regulations, 2018

Author: Chikosa M. SILUNGWE, PhD

Assignment: FAO Gcp/Glo/347/MUL

26.08.19

Date of Finalization: 10.03.20

Share on RLBI navigator
NO